Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
Rute 1:9 - Buku Lopatulika Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wake. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wake. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuthandizeni kuti mupeze pokhala, ndipo aliyense mwa inu akwatiwe.” Pompo adaŵampsompsona. Koma iwo adayamba kulira mokweza, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Yehova akuthandizeni kuti aliyense wa inu apeze pokhala pabwino komanso mwamuna.” Kenaka anawapsompsona koma awiriwo analira mokweza. |
Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
Ndipo sunandiloleze ine ndimpsompsone ana anga aamuna ndi aakazi? Wapusa iwe pakuchita chotero.
Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.
Ndipo Naomi anati kwa apongozi ake awiri, Mukani, bwererani yense wa inu kunyumba ya amai wake; Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine.
Pamenepo Naomi mpongozi wake ananena naye, Mwana wanga, kodi ndisakufunire popumulako, kuti ukhale bwino?