Ndipo pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kuchoka m'dziko la Afilisti, natuluka kukanena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu.
Rute 1:7 - Buku Lopatulika Natuluka iye kumene anakhalako ndi apongozi ake awiri pamodzi naye; nanka ulendo wao kubwerera ku dziko la Yuda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Natuluka iye kumene anakhalako ndi apongozi ake awiri pamodzi naye; namka ulendo wao kubwerera ku dziko la Yuda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho adanyamuka, pamodzi ndi apongozi akewo, kuchoka kumene ankakhala kuja, nayamba ulendo wobwerera ku dziko la Yuda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Naomi pamodzi ndi apongozi ake awiri aja anachoka kumene ankakhala ndi kuyamba ulendo obwerera kwawo ku Yuda. |
Ndipo pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kuchoka m'dziko la Afilisti, natuluka kukanena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu.
Nakweza iwo mau ao, naliranso misozi; ndi Oripa anampsompsona mpongozi wake, koma Rute anamkangamira.
Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ake kuti abwerere kuchoka m'dziko la Mowabu; pakuti adamva m'dziko la Mowabu kuti Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.
Ndipo Naomi anati kwa apongozi ake awiri, Mukani, bwererani yense wa inu kunyumba ya amai wake; Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine.