Rute 1:4 - Buku Lopatulika Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwoŵa adakwatira akazi achimowabu. Wina dzina lake anali Olipa, winayo anali Rute. Adakhala ku Mowabuko pafupi zaka khumi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anakwatira akazi a Chimowabu; wina dzina lake Oripa ndi wina Rute. Atakhala kumeneko pafupifupi zaka khumi, |
ndi Salimoni anabala Bowazi mwa Rahabu; ndi Bowazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Yese;
Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;
Ndipo musakwatitsane nao; musampatse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.
Koma Maloni ndi Kilioni anamwalira onse awiri; motero ana ake aamuna awiri ndi mwamuna wake anamsiya mkaziyo.