Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.
Rute 1:3 - Buku Lopatulika Ndipo Elimeleki mwamuna wake wa Naomi anamwalira; natsala iye ndi ana ake awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Elimeleki mwamuna wake wa Naomi anamwalira; natsala iye ndi ana ake awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Elimeleki mwamuna wa Naomi adamwalira, ndipo Naomiyo adatsala ndi ana aŵiri aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Elimeleki, mwamuna wake wa Naomi anamwalira ndipo Naomiyo anatsala ndi ana ake aamuna awiri aja. |
Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.
Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu ku Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko.
Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi.