Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Rute 1:1 - Buku Lopatulika

Ndipo masiku akuweruza oweruzawo munali njala m'dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu ku Yuda anamuka nakagonera m'dziko la Mowabu, iyeyu, ndi mkazi wake, ndi ana ake aamuna awiri.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo masiku akuweruza oweruzawo munali njala m'dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu-Yuda anamuka nakagonera m'dziko la Mowabu, iyeyu, ndi mkazi wake, ndi ana ake amuna awiri.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nthaŵi ina, pamene aweruzi ankalamulira Israele, mudaagwa njala m'dzikomo. Tsono munthu wina wa ku Betelehemu m'dziko la Yuda, adapita ndi mkazi wake ndi ana ake aŵiri, kukakhala nao mwakanthaŵi ku dziko la Mowabu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mu nthawi imene oweruza ankalamulira Israeli, munali njala mʼdziko, ndipo munthu wina wa ku Betelehemu mʼdziko la Yuda anapita pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna awiri, kukakhala ku Mowabu kwa nthawi yochepa.

Onani mutuwo



Rute 1:1
26 Mawu Ofanana  

Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m'dziko m'menemo.


Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isaki ananka kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari.


Ndipo njala inakula m'dzikomo.


Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.


Ndipo Eliya ananka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikulu mu Samariya.


Salima atate wa Betelehemu, Harefi atate wa Betegadere.


Ana a Salima: Betelehemu, ndi Anetofa, Ataroti-Beti-Yowabu, ndi Hazi Amanahati, ndi Azori.


Ndipo anaitana njala igwere dziko; anathyola mchirikizo wonse wa mkate.


Dziko la zipatso, likhale lakhulo, chifukwa cha choipa cha iwo okhalamo.


Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya onena za chilala.


Likandichimwira dziko ndi kuchita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulithyolera mchirikizo wake, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama,


Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?


Popeza ndidzathyola mphamvu yanu yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati chitsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;


Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'mizinda yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha.


Ndi pambuyo pake Ibizani wa ku Betelehemu anaweruza Israele.


Ndipo panali mnyamata wa ku Betelehemu ku Yuda, wa banja la Yuda, ndiye Mlevi, nagonera iye komweko.


Adachokera munthuyo m'mudzi mu Betelehemu ku Yuda, kugonera paliponse akapeza pokhala; ndi pa ulendo wake anafika ku mapiri a Efuremu, kunyumba ya Mika.