Numeri 7:72 - Buku Lopatulika Tsiku la khumi ndi limodzi kalonga wa ana a Asere, ndiye Pagiyele mwana wa Okarani; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku la khumi ndi limodzi kalonga wa ana a Asere, ndiye Pagiyele mwana wa Okarani; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku la 11 linali la Pagiyele mwana wa Okarani, mtsogoleri wa fuko la Asere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku la khumi ndi chimodzi, Pagieli mwana wa Okirani, mtsogoleri wa fuko la Aseri, anabweretsa chopereka chake. |
Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Asere; ndi kalonga wa ana a Asere ndiye Pagiyele mwana wa Okarani.
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Ahiyezere mwana wa Amisadai.
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;