Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazichotsa.
Numeri 7:50 - Buku Lopatulika chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazichotsa.
Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israele, ndi pakati pao panaima Yazaniya mwana wa Safani, munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m'dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera.
chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu, ndi Israele chilamulo chanu; adzaika chofukiza pamaso panu, ndi nsembe yopsereza yamphumphu paguwa la nsembe lanu.