Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.
Numeri 6:17 - Buku Lopatulika naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atatero, apereke nkhosa yamphongo kwa Chauta, kuti ikhale nsembe yachiyanjano, pamodzi ndi dengu la buledi uja wosafufumitsa. Kenaka aperekenso chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Apereke dengu la buledi wopanda yisiti ndiponso nsembe yachiyanjano kwa Yehova ya nkhosa yayimuna, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chopereka cha chakumwa. |
Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.
Ndipo wansembe azibwera nazo pamaso pa Yehova, nakonze nsembe yake yauchimo, ndi nsembe yake yopsereza;
Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wake wa kusala kwake pa khomo la chihema chokomanako, natenge tsitsi la pamutu wake wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.