Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa Iye ndi ana a Israele m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose.
Numeri 4:37 - Buku Lopatulika Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'chihema chokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'chihema chokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chimenecho ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'mabanja a Akohati, onse amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ichi chinali chiwerengero cha mafuko a Akohati onse omwe ankatumikira mu tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova. |
Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa Iye ndi ana a Israele m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose.
Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.
ndipo owerengedwa ao monga mwa mabanja ao ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.
Ndipo ana owerengedwa a Geresoni, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao,
kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa kugwira ntchito ya utumikiwu, ndiyo ntchito ya akatundu m'chihema chokomanako;
Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.