Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga.
Numeri 36:9 - Buku Lopatulika Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko, pakuti mafuko a ana a Israele adzamamatira lonse ku cholowa chakechake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko, pakuti mafuko a ana a Israele adzamamatira lonse ku cholowa chakechake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho palibe choloŵa chimene chidzachotsedwe m'fuko lina kupatsidwa ku fuko lina. Pajatu fuko lililonse la Aisraele lidzakangamira pa choloŵa chake.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Cholowa chilichonse mu Israeli sichiyenera kupita ku fuko lina, popeza fuko lililonse la Israeli liyenera kusunga cholowa chimene linalandira.” |
Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga.
Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko; popeza ana a Israele adzamamatira yense ku cholowa cha fuko la makolo ake.
Ndipo mwana wamkazi yense wa mafuko a ana a Israele, wakukhala nacho cholowa, akwatibwe ndi wina wa banja la fuko la kholo lake, kuti ana a Israele akhale nacho yense cholowa cha makolo ake.
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.