popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana aakazi a Zelofehadi, anakwatibwa ndi ana aamuna a abale a atate wao.
Numeri 36:12 - Buku Lopatulika Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo cholowa chao chinakhala m'fuko la banja la atate wao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo cholowa chao chinakhala m'fuko la banja la atate wao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakwatiwa ndi a m'mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe, ndipo choloŵa chao chidakhalabe m'fuko la bambo wao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anakwatiwa mʼmafuko a zidzukulu za Manase mwana wa Yosefe, ndipo cholowa chawo chinakhalabe mʼfuko la abambo awo. |
popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana aakazi a Zelofehadi, anakwatibwa ndi ana aamuna a abale a atate wao.
Awa ndi malamulo ndi maweruzo, amene Yehova analamulira ana a Israele ndi dzanja la Mose m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko.
Cholamulira Yehova za ana aakazi a Zelofehadi ndi ichi, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ake; komatu akwatibwe nao a banja la fuko la makolo ao okhaokha.
Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?