Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana aamuna, koma ana aakazi ndiwo; ndipo maina a ana aakazi a Zelofehadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.
Numeri 36:11 - Buku Lopatulika popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana aakazi a Zelofehadi, anakwatibwa ndi ana aamuna a abale a atate wao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana akazi a Zelofehadi, anakwatibwa ndi ana amuna a abale a atate wao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mala, Tiriza, Hogola, Milika ndi Nowa, ana aakazi a Zelofehadi, adakwatiwa ndi ana a abale a bambo wao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana aakazi a Zelofehadi amene ndi Mahila, Tiriza, Hogila, Milika ndi Nowa, anakwatiwa ndi asuweni awo a ku mbali ya abambo awo. |
Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana aamuna, koma ana aakazi ndiwo; ndipo maina a ana aakazi a Zelofehadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.
Pamenepo anayandikiza ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake aakazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.
Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo cholowa chao chinakhala m'fuko la banja la atate wao.