Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kuchita chowauza mfumu ndi akulu mwa mau a Yehova.
Numeri 36:10 - Buku Lopatulika Monga Yehova adalamulira Mose, momwemo ana aakazi a Zelofehadi anachita; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Monga Yehova adalamulira Mose, momwemo ana akazi a Zelofehadi anachita; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana aakazi a Zelofehadi adachitadi zomwe Mulungu adalamula Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho ana aakazi a Zelofehadi anachita monga Yehova analamulira Mose. |
Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kuchita chowauza mfumu ndi akulu mwa mau a Yehova.
Ndipo ana onse a Israele anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita.
Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo anatulutsa wotembererayo kunja kwa chigono, namponya miyala. Ndipo ana a Israele anachita monga Yehova adauza Mose.
popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana aakazi a Zelofehadi, anakwatibwa ndi ana aamuna a abale a atate wao.
Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko, pakuti mafuko a ana a Israele adzamamatira lonse ku cholowa chakechake.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse cholowa pakati pa abale athu; chifukwa chake anawapatsa monga mwa lamulo la Yehova, cholowa pakati pa abale a atate wao.