Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 35:3 - Buku Lopatulika

Ndipo mizinda ndiyo yokhalamo iwowa; ndi mabusa akhale a ng'ombe zao, ndi zoweta zao, inde nyama zao zonse.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo midzi ndiyo yokhalamo iwowa; ndi mabusa akhale a ng'ombe zao, ndi zoweta zao, inde nyama zao zonse.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mizindayo idzakhala yao yoti azikhalamo, ndipo mabusa ao adzakhala odyetseramo ng'ombe zao, zoŵeta zao ndi nyama zao zonse.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Midziyo idzakhala yawo ndipo azidzakhala mʼmenemo. Malo a msipu adzakhala a ngʼombe, nkhosa ndi zoweta zawo zina zonse.

Onani mutuwo



Numeri 35:3
6 Mawu Ofanana  

Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko aoao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobowamu ndi ana ake anawataya, kuti asachitire Yehova ntchito ya nsembe;


Kutengako malo opatulika akhale nayo mikono mazana asanu m'litali mwake, ndi mazana asanu kupingasa kwake, laphwamphwa pozungulira pake; ndi pabwalo pake poyera pozungulira pake mikono makumi asanu.


Uza ana a Israele, kuti apatseko Alevi cholowa chaochao, mizinda yokhalamo; muwapatsenso Alevi mabusa akuzungulira mizinda.


Ndipo mabusa a mizindayo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono chikwi chimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.


Ndipo Mlevi akachokera kumudzi wanu wina mu Israele monse, kumene akhalako, nakadza ndi chifuniro chonse cha moyo wake ku malo amene Yehova adzasankha;


Ndipo anawapatsa mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ake ozungulirapo.