Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko aoao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobowamu ndi ana ake anawataya, kuti asachitire Yehova ntchito ya nsembe;
panalinso amuna mwa ana a Aroni ansembe, okhala m'minda ya kubusa kwa mizinda yao, m'mzinda uliwonse, otchulidwa maina ao, agawire amuna onse mwa ansembe, ndi onse mwa Alevi, oyesedwa mwa chibadwidwe magawo ao.
Kuyambira tsono dziko la Alevi kufikira dziko la mzinda, ndiwo a pakati pa magawo ake a kalonga, pakati pa malire a Yuda ndi malire a Benjamini, kukhale kwa kalonga.
Ndi m'malire a Yuda, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, pakhale chopereka muchipereke, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake, ndi m'litali mwake lilingane ndi magawo enawo, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; ndi malo opatulika akhale pakati pake.
Ndipo Mlevi akachokera kumudzi wanu wina mu Israele monse, kumene akhalako, nakadza ndi chifuniro chonse cha moyo wake ku malo amene Yehova adzasankha;