Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 35:16 - Buku Lopatulika

Koma akamkantha ndi chipangizo chachitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma akamkantha ndi chipangizo chachitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Koma ngati munthu amenya mnzake ndi chitsulo, mnzakeyo nkufa, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Ndipo wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“ ‘Ngati munthu amenya mnzake ndi chitsulo, munthuyo nʼkufa, ndiye kuti iyeyo ndi wakupha ndipo wakuphayo aphedwe.

Onani mutuwo



Numeri 35:16
7 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi achigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.


Munthu akakantha munthu mnzake aliyense kuti afe, amuphe ndithu.