Numeri 35:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Mowabu, pa Yordani, ku Yeriko, ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Mowabu, pa Yordani, ku Yeriko, ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose m'zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani, ku Yeriko, kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ku zigwa za Mowabu pafupi ndi Yorodani ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti, |
Kunena za mizinda ya Alevi, nyumba za m'mizinda yaoyao, Alevi akhoza kuziombola nthawi zonse.
Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema m'zigwa za Mowabu, tsidya la Yordani ku Yeriko.
Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Mowabu pa Yordani kufupi ku Yeriko, ndi kuti,
Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko.
Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israele, kuchigono, ku zidikha za Mowabu, zili ku Yordani pafupi pa Yeriko.
Iwo ndiwo amene Yehova analamulira agawire ana a Israele cholowa chao m'dziko la Kanani.
Uza ana a Israele, kuti apatseko Alevi cholowa chaochao, mizinda yokhalamo; muwapatsenso Alevi mabusa akuzungulira mizinda.
Awa ndi malamulo ndi maweruzo, amene Yehova analamulira ana a Israele ndi dzanja la Mose m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko.
Pamenepo akulu a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazara wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele;