Ndi malire ochokera kunyanja ndiwo Hazar-Enoni, kumalire a Damasiko, ndi kumpoto kulinga kumpoto kuli malire a Hamati. Ndiyo mbali ya kumpoto.
Numeri 34:9 - Buku Lopatulika Ndipo malirewo adzatuluka kunka ku Zifuroni, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Hazara-Enani; ndiwo malire anu a kumpoto. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo malirewo adzatuluka kunka ku Zifuroni, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Hazara-Enani; ndiwo malire anu a kumpoto. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono malirewo afike mpaka ku Zifuroni, ndipo mathero ake akhale ku Hazarenani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto. |
Ndi malire ochokera kunyanja ndiwo Hazar-Enoni, kumalire a Damasiko, ndi kumpoto kulinga kumpoto kuli malire a Hamati. Ndiyo mbali ya kumpoto.
Maina a mafuko tsono ndi awa: Kuyambira nsonga ya kumpoto, ku mbali ya njira ya ku Hetiloni, polowera ku Hamati, Hazara-Enani ku malire a Damasiko kumpoto, ku mbali ya ku Hamati; ndi mbali zake zilinge kum'mawa ndi kumadzulo; Dani akhale nalo gawo limodzi.
kuchokera kuphiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kutuluka kwake kwa malire kudzakhala ku Zedadi.