Numeri 34:18 - Buku Lopatulika Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku fuko limodzi, agawe dziko likhale cholowa chao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku fuko limodzi, agawe dziko likhale cholowa chao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutenge mtsogoleri mmodzi pa fuko lililonse, kuti agaŵe dzikolo ngati choloŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo. |
Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale cholowa chanu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Iwo ndiwo amene Yehova analamulira agawire ana a Israele cholowa chao m'dziko la Kanani.
Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, zikhale zaozao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la chihema chokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.