Numeri 34:16 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anawuza Mose kuti, |
mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum'mawa, kotulukira dzuwa.
Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale cholowa chanu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Ndipo awa ndi maiko ana a Israele anawalanda m'dziko la Kanani, amene Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, anawagawira.
Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao.