ndi woyang'anira minda yampesa ndiye Simei Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yampesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifamu;
Numeri 34:10 - Buku Lopatulika Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ochokera ku Hazara-Enani kunka ku Sefamu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ochokera ku Hazara-Enani kunka ku Sefamu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mulembe malire anu akuvuma kuyambira ku Hazarenaniko mpaka ku Sefamu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu. |
ndi woyang'anira minda yampesa ndiye Simei Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yampesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifamu;
Ndi mbali ya kum'mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Giliyadi, ndi dziko la Israele, ndiwo Yordani; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum'mawa. Ndiyo mbali ya kum'mawa.
ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,
Ndipo malirewo adzatuluka kunka ku Zifuroni, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Hazara-Enani; ndiwo malire anu a kumpoto.
Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mchere, mpaka mathiriro ake a Yordani. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordani;