Ndipo anafika pa Elimu, ndi pamenepo panali akasupe a madzi khumi ndi awiri, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamanga chigono chao pomwepo pamadziwo.
Numeri 33:9 - Buku Lopatulika Ndipo anachokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adanyamuka ku Mara nakafika ku Elimu. Ku Elimuko kunali akasupe khumi ndi aŵiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi aŵiri, ndipo adamanga mahema ao kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atachoka ku Mara anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe a madzi khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa 70 ndipo anamanga misasa yawo kumeneko. |
Ndipo anafika pa Elimu, ndi pamenepo panali akasupe a madzi khumi ndi awiri, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamanga chigono chao pomwepo pamadziwo.