Numeri 33:7 - Buku Lopatulika Ndipo anachokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwake kwa Baala-Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwake kwa Baala-Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adanyamuka ku Etamu, nabwerera ku Pihahiroti, mzinda umene uli kuvuma kwa Baala-Zefoni. Ndipo adamanga mahema patsogolo pa Migidoli. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli. |
Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja.
Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.
Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga mu Mara.