lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu.
Numeri 33:56 - Buku Lopatulika Ndipo kudzakhala kuti monga ndinayesa kuchitira iwowa, ndidzakuchitirani inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kudzakhala kuti monga ndinayesa kuchitira iwowa, ndidzakuchitirani inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ndidzakuchitani inuyo zimene ndinkaganiza kuti ndiŵachite iwowo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo pamenepo ndidzachitira inu zomwe ndinaganiza kuwachitira iwowo.’ ” |
lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu.
Musamatsata miyambo ya mtundu umene ndiuchotsa pamaso panu; popeza anachita izi zonse, ndinalema nao.
Koma mukapanda kupirikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakuvutani m'dziko limene mukhalamo.
Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.
Ndipo Yehova anawazula m'nthaka mwao mokwiya ndi mozaza, ndi mu ukali waukulu, nawaponya m'dziko lina, monga lero lino.