Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.
Numeri 33:54 - Buku Lopatulika Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudzalandira dzikolo kuti likhale choloŵa chanu mwamaere, potsata mabanja anu. Fuko lalikulu lilandire choloŵa chachikulu, ndipo fuko laling'ono lilandire choloŵa chaching'ono. Dziko lililonse limene maere agwere munthu, likhale lake la munthuyo. Mudzalandire choloŵa chanu potsata mafuko a makolo anu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu. |
Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.
nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira.
Cholowa chao chinachitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mafuko asanu ndi anai ndi fuko la hafu.
Ndipo maere a fuko la ana a Benjamini anakwera monga mwa mabanja ao; ndi malire a gawo lao anatuluka pakati pa ana a Yuda ndi ana a Yosefe.