Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amowabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, paphiri lili patsogolo pa Yerusalemu.
Numeri 33:52 - Buku Lopatulika mupirikitse onse okhala m'dziko pamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mupirikitse onse okhala m'dziko pamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa mudzapirikitse nzika zonse za m'dzikomo pamene mukufika, ndipo mudzaononge miyala yao yozokota ndi kuwononganso mafano ao osungunula. Mudzasakaze akachisi ao onse ku mapiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mukathamangitse nzika zonse za mʼdzikomo pamaso panu. Mukawononge mafano awo onse a miyala ndi osula ndi malo awo achipembedzo. |
Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amowabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, paphiri lili patsogolo pa Yerusalemu.
Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.
Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umenewo; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.
Monga Yehova adalamulira Mose mtumiki wake, momwemo Mose analamulira Yoswa; momwemonso anachita Yoswa; sanachotsepo mau amodzi pa zonse Yehova adalamulira Mose.
osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kutchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;
Ndipo amuna a Israele anati kwa Ahivi, Kapena mulimkukhala pakati pa ife, ndipo tipanganenji ndi inu?
ndipo inu, musamachita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvere mau anga; mwachichita ichi chifukwa ninji?