Numeri 33:51 - Buku Lopatulika Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutaoloka Yordani kulowa m'dziko la Kanani, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutaoloka Yordani kulowa m'dziko la Kanani, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Uza Aisraele kuti, Pamene muwoloka mtsinje wa Yordani kuti muloŵe m'dziko la Kanani, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Nena kwa Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mʼdziko la Kanaani, |
Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;
Imvani Israele; mulikuoloka Yordani lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akulu ndi amphamvu akuposa inu, mizinda yaikulu ndi ya malinga ofikira kuthambo,
Ndipo ansembe akulisenza likasa la chipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordani, ndi Aisraele onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordani.