atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m'dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu.
Numeri 33:47 - Buku Lopatulika Nachokera ku Alimoni-Dibulataimu, nayenda namanga m'mapiri a Abarimu, chakuno cha Nebo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nachokera ku Alimoni-Dibulataimu, nayenda namanga m'mapiri a Abarimu, chakuno cha Nebo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adanyamuka ku Alimoni-dibulataimu, nakamanga mahema ao ku mapiri a Abarimu patsogolo pa Nebo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atachoka ku Alimoni-Dibulataimu anakamanga mʼmapiri a Abarimu, pafupi ndi Nebo. |
atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m'dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kwera m'phiri ili la Abarimu, nupenye dziko limene ndapatsa ana a Israele.
Kwera m'phiri muno mwa Abarimu, phiri la Nebo, lokhala m'dziko la Mowabu, popenyana ndi Yeriko; nupenye dziko la Kanani, limene ndipereka kwa ana a Israele likhale laolao;
Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani;