Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.
Numeri 33:39 - Buku Lopatulika Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aroniyo anali wa zaka 123 za kubadwa, pamene adamwalira pa phiri la Hori. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123. |
Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.
Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito zaka makumi anai, mwezi wachisanu, tsiku loyamba la mwezi.
Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwera m'dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israele.