Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.
Numeri 33:36 - Buku Lopatulika Nachokera ku Eziyoni-Gebere, nayenda namanga m'chipululu cha Zini (ndiko Kadesi). Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nachokera ku Eziyoni-Gebere, nayenda namanga m'chipululu cha Zini (ndiko Kadesi). Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adanyamuka ku Eziyoni-Gebere, nakamanga mahema ao m'chipululu cha Zini (ndiye kuti Kadesi). Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atachoka ku Ezioni-Geberi anakamanga ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini chimene ndi Kadesi. |
Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.
Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.
Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala mu Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.
popeza munapikisana nao mau anga m'chipululu cha Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pamadziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba mu Kadesi, m'chipululu cha Zini.
popeza munandilakwira pakati pa ana a Israele ku madzi a Meriba wa Kadesi m'chipululu cha Zini, popeza simunandipatule Ine pakati pa ana a Israele.