Ndi Segubu anabala Yairi, amene anali nayo mizinda makumi awiri mphambu itatu m'dziko la Giliyadi.
Numeri 32:40 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anapatsa Makiri mwana wa Manase Giliyadi; ndipo anakhala m'menemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anapatsa Makiri mwana wa Manase Giliyadi; ndipo anakhala m'menemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adapatsa Makiri mwana wa Manase dziko la Giliyadi, ndipo Makiriyo adakhala m'dziko limenelo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Mose anapereka Giliyadi kwa Amakiri, ana a Manase, ndipo anakhala kumeneko. |
Ndi Segubu anabala Yairi, amene anali nayo mizinda makumi awiri mphambu itatu m'dziko la Giliyadi.
Ndipo dziko ili tinalilanda muja; kuyambira ku Aroere, wa ku mtsinje wa Arinoni, ndi dera lina la ku mapiri a Giliyadi, ndi mizinda yake, ndinapatsa Arubeni ndi Agadi.
Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.