Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu mu Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu mu Hamu, ndi Aemimu mu Savekiriyataimu,
Numeri 32:37 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Kiriyataimu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Kiriyataimu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Rubeni adamanga mizinda ya Hesiboni. Eleyale, Kiriyataimu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Arubeni anamanga Hesiboni, Eleali, Kiriataimu, |
Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu mu Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu mu Hamu, ndi Aemimu mu Savekiriyataimu,
Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m'kati mwake.
Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.
Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.
chifukwa chake taona ndidzatsegula pambali pake pa Mowabu kuyambira kumizinda, kumizinda yake yokhala mphepete, yokometsetsa ya m'dziko, Beteyesimoti, Baala-Meoni, ndi Kiriyataimu,
Chifukwa chake iwo akunena mophiphiritsa akuti, Idzani ku Hesiboni, mzinda wa Sihoni umangike, nukhazikike.
Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,
ndi Nebo, ndi Baala-Meoni (anasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaitcha mizinda adaimanga ndi maina ena.