Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordani, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Giliyadi likhale laolao;
Numeri 32:30 - Buku Lopatulika koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko aoao pakati pa inu m'dziko la Kanani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko aoao pakati pa inu m'dziko la Kanani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma akapanda kuwoloka nanu, atatenga zida zankhondo, adzalandira chuma chao pakati panu m'dziko la Kanani.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati sawoloka pamodzi nanu ndi zida zankhondo, ayenera kulandira cholowa chawo pamodzi ndi inu ku Kanaani. |
Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordani, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Giliyadi likhale laolao;
Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzachita.
Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m'dziko la cholowa cha Yehova m'mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.