koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga.
Numeri 32:28 - Buku Lopatulika Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a makolo a mafuko a ana a Israele za iwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a makolo a mafuko a ana a Israele za iwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Mose adalamula wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mabanja a mafuko a Aisraele kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Mose anapereka malamulo awa kwa wansembe Eliezara, kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa akulu a mafuko a Aisraeli. |
koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga.
Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordani, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Giliyadi likhale laolao;
Kumbukirani mau amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani inu, kuti, Yehova Mulungu wanu akupatsani mpumulo, nadzakupatsani dziko lino.