Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzachita monga mbuyanga alamulira.
Numeri 32:26 - Buku Lopatulika Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng'ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m'mizinda ya ku Giliyadi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng'ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m'midzi ya ku Giliyadi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana athu ndi akazi athu atsala ku mizinda ya Giliyadi, pamodzi ndi nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu zomwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana ndi akazi athu, ziweto zathu zina ndi ngʼombe zidzatsala kuno ku mizinda ya Giliyadi, |
Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzachita monga mbuyanga alamulira.
Koma akazi anu, ndi ana anu, ndi zoweta zanu, (ndidziwa muli nazo zoweta zambiri), zikhale m'mizinda yanu imene ndinakupatsani;
Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m'dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordani; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza;
Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.