Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka; nsalu zotchinga za dziko la Midiyani zinanjenjemera.
Numeri 31:7 - Buku Lopatulika Ndipo anawathira nkhondo Amidiyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anawathira nkhondo Amidiyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraelewo adamenyana nkhondo ndi Amidiyani, monga momwe Chauta adaalamulira Mose, ndipo adapha amuna onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anamenyana ndi Amidiyani monga momwe Yehova analamulira Mose ndipo anapha mwamuna aliyense. |
Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka; nsalu zotchinga za dziko la Midiyani zinanjenjemera.
Ndipo chimene mukachite ndi ichi: mukaononge konse mwamuna aliyense, ndi mkazi aliyense wodziwa mwamuna mogona naye.
Pamenepo Amidiyani onse ndi Aamaleke ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'chigwa cha Yezireele.
Ndipo Davide anapasula dzikolo, sanasunge ndi moyo mwamuna kapena wamkazi; natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi ngamira, ndi zovala; nabwera nafika kwa Akisi.