mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.
Numeri 31:54 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golide kwa akulu a zikwi ndi a mazana, nalowa naye ku chihema chokomanako, chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golide kwa akulu a zikwi ndi a mazana, nalowa naye ku chihema chokomanako, chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose ndi wansembe Eleazara adalandira golideyo kwa atsogoleri a ankhondo zikwi ndi a ankhondo mazana, namuika m'chihema chamsonkhano, kuti akhale chikumbutso cha Aisraele pamaso pa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose ndi Eliezara wansembe analandira golide kuchokera kwa atsogoleri a 1,000 ndi atsogoleri a 100 ndi kukamuyika mu tenti ya msonkhano ngati chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova. |
mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.
Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.
Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.
Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.
Ndipo akorona adzakhala wa Helidai, ndi wa Tobiya, ndi wa Yedaya, ndi wa Heni mwana wa Zefaniya, akhale chikumbutso mu Kachisi wa Yehova.
chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.
Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.
Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.
Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.