Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 31:53 - Buku Lopatulika

Popeza wankhondo yense anadzifunkhira yekha.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Popeza wankhondo yense anadzifunkhira yekha.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

(Ankhondo aja anali atatenga zofunkha, aliyense zakezake.)

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Wankhondo aliyense anatenga zomwe analanda yekha ku nkhondo.

Onani mutuwo



Numeri 31:53
5 Mawu Ofanana  

Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka.


Ndipo zakunkhondo, zotsalira zofunkha zonse adazifunkha ankhondowa, ndizo nkhosa zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zikwi makumi asanu ndi awiri kudza zisanu,


Ndipo golide yense wa nsembe yokweza ya Yehova amene anapereka kwa Yehova, wofuma kwa atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo masekeli zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.


Ndipo ana a Israele anagwira akazi a Amidiyani, ndi ana aang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi chuma chao chonse.


Koma akazi ndi ana ndi ng'ombe ndi zonse zili m'mzindamo, zankhondo zake zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani.