Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.
Numeri 31:51 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golideyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golideyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Mose ndi wansembe Eleazara adalandira golide kwa atsogoleriwo, pamodzi ndi zinthu zonse zosula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara analandira kuchokera kwa atsogoleriwo golide pamodzi ndi zipangizo zonse zosula. |
Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.
Ndipo golide yense wa nsembe yokweza ya Yehova amene anapereka kwa Yehova, wofuma kwa atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo masekeli zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.