Numeri 31:5 - Buku Lopatulika Ndipo anapereka mwa zikwi za Israele, a fuko limodzi chikwi chimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapereka mwa zikwi za Israele, a fuko limodzi chikwi chimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho pa anthu a Aisraele ambirimbiri aja, Mose adatumiza anthu chikwi chimodzi pa fuko lililonse, ndipo onse anali 12,000 pamodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho amuna okwana 12,000 anatenga zida kukonzekera nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli. |
Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake.