Numeri 31:27 - Buku Lopatulika nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anatuluka kunkhondo, ndi khamu lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anatuluka kunkhondo, ndi khamu lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo mugaŵe zofunkhazo magawo aŵiri, lina la ankhondo amene adaapita ku nkhondo, lina la mpingo wonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mugawe zolanda ku nkhondozo magawo awiri, lina la ankhondo amene anapita ku nkhondo, lina la anthu onse. |
Pogona inu m'makola a zoweta, mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.
Werengani zakunkhondo, ndizo anthu, ndi zoweta, iwe, ndi Eleazara wansembe, ndi akulu a nyumba za makolo za khamulo;
nanena nao ndi kuti, Bwererani nacho chuma chambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndi siliva, ndi golide, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi malaya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu.
Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.