Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a chitsulo; mlongo wake wa Tubala-Kaini ndi Naama.
Numeri 31:22 - Buku Lopatulika Golide, ndi siliva, mkuwa, chitsulo, ndolo ndi mtovu zokha, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Golide, ndi siliva, mkuwa, chitsulo, ndolo ndi mtovu zokha, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Izi zokha, golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, chiwaya ndi mtovu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Golide, siliva, mkuwa, chitsulo, chiwaya, mtovu |
Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a chitsulo; mlongo wake wa Tubala-Kaini ndi Naama.
Ndipo Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga onse a khamulo, anatuluka kukomana nao kunja kwa chigono.
Ndipo Eleazara wansembe ananena ndi ankhondo adapita kunkhondowo, Lemba la chilamulocho Yehova analamulira Mose ndi ili:
zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi.
Koma siliva yense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m'mosungira chuma cha Yehova.
Koma ng'ombe ndi zofunkha za mzinda uwu Israele anadzifunkhira monga mwa mau a Yehova amene analamulira Yoswa.