Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, pakati pa atate ndi mwana wake wamkazi, akali namwali, m'nyumba ya atate wake.
Numeri 31:21 - Buku Lopatulika Ndipo Eleazara wansembe ananena ndi ankhondo adapita kunkhondowo, Lemba la chilamulocho Yehova analamulira Mose ndi ili: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Eleazara wansembe ananena ndi ankhondo adapita kunkhondowo, Lemba la chilamulocho Yehova analamulira Mose ndi ili: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono wansembe Eleazara adauza ankhondo amene adaapita ku nkhondowo kuti, “Lamulo limene Chauta walamula Mose ndi ili: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono wansembe Eliezara anati kwa asilikali amene anapita ku nkhondo aja, “Lamulo limene Yehova anapereka kwa Mose ndi ili: |
Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, pakati pa atate ndi mwana wake wamkazi, akali namwali, m'nyumba ya atate wake.
Muyeretse zovala zanu zonse, zipangizo zonse zachikopa, ndi zoomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse za mtengo.