Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.
Numeri 31:14 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anakwiya nao akazembe a nkhondoyi, atsogoleri a zikwi, atsogoleri a mazana, akufuma kunkhondo adaithira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anakwiya nao akazembe a nkhondoyi, atsogoleri a zikwi, atsogoleri a mazana, akufuma kunkhondo adaithira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Mose adakwiyira akulu ankhondowo, atsogoleri olamulira ankhondo zikwi ndiponso atsogoleri olamulira ankhondo mazana, amene ankachokera ku nkhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anakwiya nawo akuluakulu a magulu a ankhondowo: olamulira 1,000 ndi olamulira 100, amene ankachokera ku nkhondo. |
Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.
Niti kwa iye, Atero Yehova, Popeza wataya m'dzanja lako munthu uja ndinati ndimuononge konse, moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wake, ndi anthu ako m'malo mwa anthu ake.
Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.
Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri.
Ndipo Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yauchimo, ndipo taonani, adaitentha. Ndipo anapsa mtima pa Eleazara ndi Itamara, ana otsalawo a Aroni, nati,
Ndipo Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga onse a khamulo, anatuluka kukomana nao kunja kwa chigono.
Pamenepo akazembe a pa ankhondo zikwi, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, anayandikiza kwa Mose;
idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta.