Numeri 31:11 - Buku Lopatulika Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa natenga zonse zimene adalanda kunkhondoko, anthu pamodzi ndi nyama zomwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anatenga zonse zimene analanda ku nkhondoko, anthu ndi zoweta zomwe. |
Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israele, kuchigono, ku zidikha za Mowabu, zili ku Yordani pafupi pa Yeriko.
Koma akazi ndi ana ndi ng'ombe ndi zonse zili m'mzindamo, zankhondo zake zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani.
Ndi zofunkha zonse za mizinda iyi ndi ng'ombe ana a Israele anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya.
Koma siliva yense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m'mosungira chuma cha Yehova.
ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng'ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mzinda.