Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.
Numeri 3:35 - Buku Lopatulika Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja la Merari ndiye Zuriyele mwana wa Abihaili; azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumpoto. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja la Merari ndiye Zuriyele mwana wa Abihaili; azimanga mahema ao pa mbali ya Kachisi ya kumpoto. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo munthu amene anali mutu wa mabanja a Merari anali Zuriyele mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga zithando zao kumpoto kwa chihema cha Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Amerari anali Zuriyeli mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga misasa yawo kumpoto kwa Chihema. |
Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.
Mbendera ya chigono cha Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai.
Ndipo owerengedwa ao, powerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi zisanu ndi chimodzi kudza mazana awiri.
Ndipo choyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a chihema, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake, ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito zake zonse;