Numeri 3:33 - Buku Lopatulika Banja la Amali, ndi banja la Amusi ndiwo Amerari; ndiwo mabanja a Merari. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Banja la Amali, ndi banja la Amusi ndiwo a Merari; ndiwo mabanja a Merari. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amali ndi Amusi anali mabanja otuluka mwa Merari. Ameneŵa ndiwo amene anali mabanja a Merari. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwa Merari kunali banja la Mali ndi banja la Musi. Amenewa ndiye anali mabanja a Amerari. |
Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao ndi awa.
Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akora. Ndipo Kohati anabala Amuramu.
Ndi ana a Merari monga mwa mabanja ao: Mali ndi Musi. Awa ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.
Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pamalo opatulika.
Ndipo owerengedwa ao, powerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi zisanu ndi chimodzi kudza mazana awiri.
Kunena za ana a Merari, Uwawerenge monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao.