ndiyo nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata lililonse, pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.
Numeri 29:34 - Buku Lopatulika ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi zachakumwa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. |
ndiyo nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata lililonse, pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.
ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa yamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;
Tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamachita ntchito ya masiku ena;