Ndi tsiku lachisanu ndi chimodzi ng'ombe zisanu ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;
Numeri 29:30 - Buku Lopatulika ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. |
Ndi tsiku lachisanu ndi chimodzi ng'ombe zisanu ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;
ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.