Ndi tsiku lachitatu ng'ombe khumi ndi imodzi, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi opanda chilema;
Numeri 29:21 - Buku Lopatulika ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pamodzi ndi zopereka zake zachakudya ndi za chakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. |
Ndi tsiku lachitatu ng'ombe khumi ndi imodzi, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi opanda chilema;
ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.
pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.